ZOPEREKA KUTHUMBA (#13494)

Abwenzi onse a Mulungu …… ayenera kusonkha monga momwe angathere, chingakhale pang’ono chabe. Mulungu sakakamiza aliyense kupambana zomwe ali nazo. Zosonkhazi ziyenera kuchokera ku madera ali onse ndi kwa wokhulupirira aliyense …..  
O abwenzi a Mulungu! Khulupirani motsimikiza kuti mmalo mwa zoperekazi, minda yanu, mafakitale anu, ndi mabizinesi anu adzadalitsika kwakukulu, ndi mphatso zokoma ndi chaulere. Iye amene abwera ndi ntchito yabwino kamodzi adzalandira mphotho kakhumi. Palibe kukayika kuti Ambuye wamoyo adzalimbikitsa mowirikiza iwo amene agwiritsa ntchito chuma chawo mu njira Yake.  
 
 O Mulungu, Mulungu wanga! Walitsani zikope za wokondeka Anu oona ndipo muwathandize ndi makamu a angelo mkupambana kosapeneka. Limbikitsani mapazi awo mu njira Yanu yowongoka, ndipo kuchokera ku chaulere Chanu chakalekale atsekulireni makomo amadalitso Anu; chifukwa akugwiritsa ntchito chuma chawo munjira Yanu yomwe Inu Mudawapatsa, kuchinjiriza Chikhulupiliro Chanu, kuyika chikhulupiliro chawo m’kukumbukira Inu, ndi kusagwiritsitsa chomwe ali nacho chifukwa cha kupembedza Kukongola Kwanu ndi kufunafuna kwawo njira zokusangalatsirani Inu.  
O Ambuye wanga! Agawireni gawo lawo lopambana, mphatso yosankhidwa ndi malipiro osakayikira. Ndithudi, Inu Ndinu Mchinjirizi, Mthandizi, Osaumira, Wachaulere, Wopatsa Nthawi Zonse.

-`Abdu'l-Bahá
-----------------------

